AWONJEZELA NGWILIZANO
BOB MPINGANJIRA NDI MCDONALD NGINDE MTETEMELA ADAKALIBE NDI MANOMA Timu ya Mighty Wanderers FC yawonjezela Mgwilizano wake aphunzisi awiri a timuyi Kwa Zaka ziwiri zikubwelazi. Malingana ndi tsamba la nchezo la team yi lapa Facebook, Mphunzisi wankulu wa team yi Bob Mpinganjira ndi wachiwiri wawo a McDonald Nginde Mtetemela akhalabe akuphunzisa team yi mpaka 2028 Anthu ambiri akukhulupilila kuti izi zachitika chifukwa cha ntchito yabwino yomwe awiriwa agwira ku team yi yobwelesa chikho cha TNM Super League chaka chino. Ma team amu League yayikulu ya mziko muno ali ali kalikiliki kukomzekela season ya 2026 Wolemba: Steven Pangani