MITENGO YOLOWELA PA ZIPATA YATULUSIDWA
Football Association of Malawi (FAM) yatulutsa mitengo ya masewero a ndime yosiliza ya Castel Challenge Cup pakati pa matimu a Goshen City Dedza Dynamos ndi FCB Nyasa Big Bullets omwe alipo loweruka likudzali pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.
Tikiti ya open ikugulitsidwa K6000 ndipo tsiku la masewerowa anthu azagula K10, 000.
Tikiti ya VIP ikugulitsidwa K10, 000 pomwe pa tsiku la masewerowa anthu azagula K15, 000.
Corporate Box yomwe imalowa anthu khumi ikugulitsidwa K200, 000.
Matikitiwa akuganizilidwa malo osiyana-siyana mu nzinda wa Lilongwe
Aka akhala koyamba Kuti timu ya Goshen City Dedza Diamonds ilaweko ndalama zamu Castel Challenge Cup.
Wolemba: Steven Pangani
Source: Football Association of Malawi

Comments
Post a Comment