WOSEWELA APAMWAMBA ALIPO
A MPINGANJIRA ATSIMIKIZA KUTI TEAM YAWO ILI NDI OSEWELA APAMWAMBA OMWE ANGATHE KUMENYA CAF CHAMPIONS LEAGUE
Pulezidenti watimu ya Mighty Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira wati timuyi ili ndi osewera a pamwamba omwe ali ndikuthekera kochita zakupsa m'mipikisano yosiyanasiyana ya m'dziko muno kuphatikizapo ya kunja monga yokonzedwa ndi CAF.
A Mpinganjira alankhula izi pomwe amatsimikiza kuti timuyi isewera nawo mumpikisano wa CAF Champions League wa chaka chino kufikira chaka cha mawa.
Wanderers isewera CAF Champions League potsatira kukhala akatswiri a ligi yaikulu ya m'dziko muno ya Supa Ligi.
Chaka chatha team ya Mighty Wanderers FC inatenga nawo gawo mu CAF confederation cup kamba kokhala akatsiri a Mpikisano wa Castel Challenge Cup wa chaka cha 2024.
Wolemba: Steven Pangani

Nice one brother 🤲🏼
ReplyDelete