WABWELERA

KUCHEDWA KWA CHIPHASO CHOYENDELA KWASOKONEZA ZINTHU 

Otchinga pagolo wakale wa matimu a Bangwe All Stars, Ekhaya FC komanso FCB Nyasa Big Bullets Reserve, Elias Missi, wabwerera kumudzi kuchokera ku timu ya Dynamos FC yaku Zimbabwe kamba kakuchedwa kutuluka kwa chiphanso chake choyendera.

Missi anapita kutimuyi komwe amachita zokonzekera ndi anzake pogwiritsa ntchito pepala ngati chilolezo cholowera m'dzikoli.

Koma kutatsala pang'ono kuti ligi yaikulu ku Zimbabwe iyambe, akulu-akulu a timuyi anamuuza kuti akatenge chitupa choyendera ndicholinga choti amulembe ntchito.

"Amwene zandivuta kamba koti passport yanga inali isanatuluke. Koma akulu-akulu a timuyi anditsimikizira kuti andiitananso chaka cha mawa.

"Nditsimikize pano kuti nditumikira kunkuno potengera kuti matimu ena ayamba kale kugogoda," watero Missi.

Wolemba: Steven Pangani 

Source: TimveniSportsDesk

Kanema: Kuwonesa zochitika Za Elias Misi




Comments

Popular posts from this blog

MWAMBO UWONESEDWA PA KANEMA

ON THE WAY TO WOMEN FIFA U20

IRAN WITHDRAW FIFA WORLD CUP